Timu ya ngakhale anakwanitsa kukwapula Manchester United mowitikiza chaka chino.
M’masewero awo a mu chikho cha Premier League, Ange Postecoglou anagagada ma Devils masewero a pakhomo komanso kwawo kwa Manchester United, kuja ku Old Trafford.
Mu EFL Cup, Ange Postecoglou anaipakiritsa Manchester United mu ndime ya quarter-finals poyisasantha Manchester United 4-3.
Mu ndime yomaliza ya UEFA Europa League Ange Postecoglou anayiwonetsa United chinameta nkhanga mpala, poyikazingira 1-0, kuti Tottenham ipeze chikho choyamba kuchokera m’chaka ch 1984.
Komabe Spurs yamaliza pa nambala 17 mu sizoni ya 2024/2025 ndi ma poinsi 38 mu maseweronso 38 omwe yasewera, kukwapulidwa mu masewero ake 22 zimene sizinakondweretse mabwana ku Board ndipo Ange Postecoglou amuwonetsa nsana wa njira.